No | Nseketso | Matanthauzo |
1. | Ndimayikanyanga m'nyumbamu. |
Ndimadya nsima m'nyumbamu.
Ndimayika mankhwala aufiti m'nyumbamu. |
2. | Kholowa m'kabudula amamera? |
Kodi kholowa mukamudula amamera?
Kodi kholowa m'kati mwa kabudula amamera? |
3. | Kodi zimathamanga ng'ombezo m'kasaka? |
Kodi ng'ombe zimathamanga m'kazisaka?
Kodi ng'ombe zimathamanga m'saka?
|
4. | Kodi ufa ukadya? |
Kodi umwalira ukadya?
Kodi ufa wachimangawu ukadya?
|
5. | Kodi nkhuku m'katsekera zimatuluka? |
Kodi nkhuku zikakhala monga m'khola ndi kutseka
kukhomo kwa kholalo, nkhukuzo zimatuluka?
Kodi nkhuku zikakhala mu tsekera zimatuluka? |
6. | Kodi zaka zako ndi zaka zanga n'zofanana? |
Kodi za akazi ako ndi akazi anga ndi zofanana?
Kodi zaka zako ndi zaka zanga n'zofanana? |
7. | T'ikumana kukachaso. |
Tikumana ku kacha m'mawa.
Tikumana ku malo omwera mowa wa kachasu.
|