Download Android app Mizembaitso

MIZIMBAYITSO

  • Mzimbayitso ndi mawu onena nkhani mopanda chindunji; kapena tinene kuti mophiphiritsa.

  • Mizimbayitso ilipo yosiyanasiyana ndipo ina mwa iyo ndi iyi:

    (a) Mizimbayitso yonyoza
  • Iyi ndi mizimbayitso ya matanthauzo onyoza.

  • Poyankhula munthu amachita ngati akuyamikira, pomwe m'maganizo ake muli kunyogodola kapena kuyipitsa.
  • Zitsanzo:

    MzembaitsoTanthauzo
    Chisotichi chakukhala bwino kuyamikira monama pamene munthuyo chisoticho sichidamukhale bwino
    Koma ndiye ndiwozi wazikazinga bwino kwambirikuyamikira monama pamene ndiwozo sadakazinge bwino

    (b) Mizimbayitso yonyalapsa

  • Mawu onyalapsa amanenedwa ndi cholinga chopereka ulemu kapena kuchepetsa nthumanzi kapenanso mantha omwe munthu ali nawo.


  • Munthu amanena mwaulemu kapena mosafuna kutchula mawu omwe akhoza kusonyeza ngati mawu achipongwe kapena opanda ulemu kapena otukwana kapenanso ochititsa phuma.

  • Zitsanzo:
    Mizimbayitso yonyalapsaTanthauzo
    Abambo aja atisiyaAbambo amwalira
    Mwana wapambuka Mwana wanyera kapena wasoma.
    Mwana wayipitsira pano Mwana wanyera kapena wasoma.
    Ndifuna ndikataye madzi Ndifuna ndikakodze.
    Ndinapita kukayimiriraNdinakakodza.
    Nambewe ngodwala Nambewe akuyembekezera kubala mwana.
    Mkaziyu ngoyendayendaMkaziyu ndi wachiwerewere, hule kapena wadama.
    Mnyamata chamuyambwa chitedzeMnyamata watenga nthenda chifukwa cha chiwerewere.
    Mayiyu wapita padera Mayiyu wabala mwana wakufa.
    Mtsikanayu ali ndi pakatiMtsikanayu ali ndi mimba.