NKHAMBAKAMWA
Nkhambakamwa ndi nkhani yongonena zinthu mocheza chabe kapenanso
zopanda nazo umboni, ndipo mwina sizingachitikenso choncho ngakhale
zikuyankhulidwa.
Nthawi zina munthu amayankhula zakale ngakhale kalero
sizidali choncho kwenikweni kumbali yake.
Munthu amangoyankhula
pofuna kusonyeza kuti sadali umo alili tsopano.
Mawu ena amanena
pongofuna kuwopseza kapena kuwonjezera kapenanso kukometsa chabe.
Zitsanzo:
Ana inu, tidali atsikana ife kale.
- anali okongola, pomwe mwina sadali wotero)
Ndidali munthu ine masiku amenewo.
- adali wowoneka bwino kapena wachuma pomwe
mwina adalibe chilichonse
Ndimkati ndikamenya munthu kuferatu.
- adali ndi mphamvu zambiri pamene mwina sadali
choncho.
Sunganditero ine! Uwona.
- ndi wowopsa kapena wosati n'kusewera naye pamene
mwina sali choncho.
Tinkamenyatu ife, tili anyamata.
- adali ndi mphamvu zambiri pamene mwina adalibe
mphamvu zambiri