Ntchedzero

  • Ntchedzero ndi mawu omwe matanthauzo ake ndi oserewula mwina oseketsa.
  • Palinso ntchedzero zina zomwe matanthauzo ake ndi okwiyitsa kapena opsetsa mtima.
  • Ponena ntchedzero anthu amafananitsa munthu ndi chinthu china chake pogwiritsa ntchito mawu woti 'ngati' kapena 'monga'.
  • Izi zikusonyeza kuti ndi kofunika kuzindikira kuti ntchedzero ndi mtundu wa zifanifani.
  • Zitsanzo:

    Ntchedzero Tanthauzo
    timawu ngati mngoli mawu okongola zedi poyimba kapena poyankhula
    kuwala ngati nyenyezi mawonekedwe osagalatsa
    kutsekemera monga uchi kuzuna kwambiri kwa chinthu
    kuwawa ngati ndulu ya ng'ona kuwawa kwambiri kwa zakudya kapena zakumwa
    kuswana ngati dzombe kuchulukana kwambiri kwa zinthu
    chifundo monga cha msemamitondo kukhala ndi chifundo chachikulu chopezetsa mavuto munthu womverera chifundo mnzakeyo

    Ntchedzero zachilengo

  • Ntchedzero ya chilengo ndi mawu ochedzera munthu kapena chinthu monyoza.

  • Mawuwa amapsetsa mtima mpaka mwina anthu akhoza kumenyana kapena kukwiyirana chifukwa chonenana chilema kapena mawonekedwe oyipa a wina ndi mnzake.

  • Zilengo nazonso ndi mtundu wa zifanifani popeza zimasonyeza kufananitsa zinthu.

  • Zitsanzo:
    Ntchedzero za Chilengo Tanthauzo
    Chimutu kukula ngati mdenga mutu waukulu kwambiri
    Kuda ngati makala kuda kwambiri
    Kuda monga kuseri kwa m'phika kuda kwambiri
    Kuda monga chikuni chowawuka ndi moto kuda kwambiri
    Mawu ngati chule mawu oyipa makamaka poyimba
    Mphuno ngati chikololo cha azungu mphuno yaitali

    Kusintha ntchedzero/zifanifani kukhala zining'a

  • Kumatheka kusintha ntchedzero/chifanifani kuti zikhale zining'a makamaka pamene tikufanizira chinthu china ndi chinzake.

  • Kufaniziraku kukhoza kuchitika moganizira mawonekedwe, machitidwe, mamvekedwe kapena makhalidwe a zinthu zomwe tikukambira nkhani.

  • Zitsanzo:
    Zifanifani Zining'a zake
    Ndiwe wokongola ngati nyenyezi ndiwe nyenyezi
    Ndiwe wochenjera ngati kalulu ndiwe kalulu
    Ndiwe wakuda ngati mtsiro ndiwe mtsiro
    Ndiwe wonunkha ngati kanyimbi ndiwe kanyimbi
    Ndiwe wopusa ngati mbuzi ndiwe mbuzi
    Ndiwe womveka kwambiri ngati ng'oma ndiwe n'goma
    Ndiwe wabodza ngati mthirakuwiri ndiwe nthirakuwiri
    Ndiwe wamantha ngati fisi ndiwe fisi
    Ndiwe wokonda kukhala m'nyumba ngati thunga ndiwe thunga.
    Ndiwe wosadziwa kusambira ngati mbiya ndiwe mbiya



    Developed by Welford Khodo Kuthakwaanthu