VOKO
Voko ndi mawu onena mowonjezera kapena mosinjirira chabe pamene
zonenedwazo sizili choncho kwenikweni ayi.
Zitsanzo:
a) Ku ukwatiko kudalibe ndi munthu yemwe.
- Akunena izi pamene anthu angapo adaliko ku ukwatiko.
b) Kuli chimunthu chamnanu kumsonkhanoko.
- Akunena izi pamene kuli anthu owerengeka chabe.
c) Mwana wanga kusukulu dzina n'lake lokha
- Akunena izi pomwe mwanayo sadachite kutchuka kwenikweni
kusukuluko
d) Panalibenso wina woyimba bwino ndine ndekha.
- Akunena izi pomwe ena oyimba bwino kuposa iye analiko)
e) M'dengu muli gwa mopanda ndi ufa womwe.
- Akunena izi pamene ufa ulimo pang’ono woti n’kukwanira
kuphikira nsima yochepa
f) Zovala zonse zijatu n'zogula ine.
- Akunena izi pomwe iye adagula chovala chimodzi kapena ziwiri
zokha