MIKULUWIKO

KODI MKULUWIKO NDI CHIYANI?


  • Mkuluwiko ndi mawu okhala ndi tanthauzo lobisika kapena lophiphiritsa.

  • Timanena mkuluwiko pofuna kubisa tanthauzo la zomwe tikunena kuti ana kapena ena, asadziwe zomwe tikunena.
  • Nthawi zina timanena mkuluwiko pofuna kungokometsa nkhani kukhala ngati nsinjiro zotenderera nkhaniyo kuti ikome.
  • Mkuluwiko nthawi zambiri umakhala chiganizo.
  • Tidziwenso kuti mkuluwiko ndi mutu wa mwambi kapena nkhani kapenanso nthano.
  • Mkuluwiko uliwonse uli ndi nkhani, nthano kapena mwambi wake womwe, tinganene kapena kufotokoza.

  • Zitsanzo za mikuluwiko ndi matanthauzo ake

    Mkuluwiko

    Tanthauzo

    Tikonzetikonze adanyula maliro aeni.

    Munthu usamajijirika pa zinthu za eni chifukwa ukhoza kupezeka pavuto lina lake utalakwitsa china chake.

    Ulenje umasimba wako.

    Munthu uzisimba zokhudza iwe osati zokhudza anthu ena.

    Galu wamkota sakandira pachabe.

    Wamkulu akamanena kapena kuchita zinthu sangochitapo chabe mopanda kudziwa chomwe akunena kapena kuchita.

    Kunena kwa ndithendithe nanthambwe adadzitengera.

    Si bwino kufulumira kuwulula zinsinsi za ena chifukwa kuteroko ukhoza kupalamula nako.

    Tsabola wakale sawawa.

    Zakale zilibe ntchito.

    Mawu aakulu akoma akagonera.

    Nzeru za aakulu zimawoneka phindu lake pakapita nthawi.

    Patsala paja pagona chinziri.

    Kunena nkhani zakale pofuna kukometsa zinthu pa mlandu.

    Chetechete sawutsa nyama.

    Kungokhala chete sikupindula kanthu ngati munthu akufuna kukwaniritsa chimene akufuna.
    Ntchenzi idamva mawu oyamba.
  • Mawu oyamba ndiwo amene anthu amawerengera kuti ndiwo mawu onena zowona.
  • Kulamula vumbwe n'kulinga uli ndi nkhuku.
  • Munthu usamapalamula pamene ulibe populumukira.
  • Tsoka nsinde chimanga chilinda moto.
  • Kuchita tsoka lalikulu.
  • Ili kutali mvula mpesa umera ng'amba.
  • Zinthu kumachitika panthawi yake mosatengera kuti wina kapena china chake palibe.
  • Mlendo ndi amene adza n'kalumo kakuthwa.
  • Mlendo akhoza kuthandiza pa vuto lomwe eni mudzi angakhale nalo.
  • Mbuto ya kalulu idakula n'tadzawonani.
  • Anthu ena amakuza nkhani mowonjezera chabe kapena ponena zabodza.
  • Makale sapanganika, adalira m'thumba la mbala.
  • Kamakhalapo kanthu kowululitsa zobisika kapena zachinsinsi
  • Khoswe wapadenga/patsindwi adawululitsa wapadzala.
  • Chinthu china chimawululitsa chomwe chinali chobisika.
  • Mthanga kunena adapisa likogwe wa apongozi.
  • Tisamalonjeza msanga za chinthu chomwe sitingachikwaniritse.
  • Wakufa sadziwika.
  • Wogonja kapena wopambana sadziwika mpaka pothera pake
  • Chifundo chidapha msemamitondo.
  • Chifundo nthawi zina chimapweteketsa.
  • Nyama yaliwuma idafa ndi ludzu.
  • Liwuma limapweteketsa.
  • Maso aipsa, kamwa likonza.
  • Choyipa m'mawonekedwe nthawi zina chimakhala chokoma ukachidya.
  • Nyalugwe chepsa cha mnzake, iye akapha chiwala achita chokoka.
  • Pali anthu ena okonda kunyoza za anzawo nthawi zonse koma amakometsa zawo zokha ngakhale zikhale zoyipa.
  • Nyumba ya mwini sawotchera mbewa.
  • Osamadalira kwambiri zinthu za eni.
  • Nguluwe idalira msampha utaning'a.
  • kuyamba kudandaula vuto litakhala pang'ono kutha.
  • Ukatchula mkango kwera m'mwamba.
  • Ukamanena za munthu ndiye kuti munthuyo ali pafupi kufika pamalopo kotero ndi bwino kukonzekera njira yodzipulumutsira nayo iyeyo atakumva zomwe uli kunena za iye.
  • Suzumire adaphetsa mkhalakale.
  • Kusaugwira mtima kumadzetsa mavuto.
  • (a) Wamuwonetsa chidameta mduliro nyani.
  • (b) Wamuwonetsa chidameta nkhanga mpala.
  • Wamukhaulitsa
  • Lungalunga mpobadwa chilema chichita kudza.
  • Vuto la pathupi limachita kubwera.
  • Linda madzi apite ndipo uziti ndadala.
  • Si bwino kudzitama vuto lisanafike posonyeza kuti latha.
  • Ndawonera momwemu mwambi wa gulugufe.
  • Kukhutira ndi zomwe uli nazo.
  • Nkhuyu zodya mwana zidapota akulu.
  • Mavuto opalamula ana amavutitsa makolo awo.
  • Kumbire adamka nawo kumanda.
  • Si bwino kuzolowera kuchitiridwa chilichonse popeza nthawi ina udzasowa wokuthandiza pamene yemwe amakuthandiza palibe.
  • Wokoma atani wonga fungwe.
  • Kudandawulira anthu osayamika ngakhale uwachitire chabwino.
  • Ndim'khulupirira adam'gonetsa m'nkhufi.
  • Munthu womudalira nthawi zina ndi amene amakukhumudwitsa kwambiri.
  • Mwana wa pang'ona salephera kuyangala.
  • Nthawi zambiri mwana amatengera luso kapena khalidwe kuchokera kwa makolo ake.
  • Tsoka sasimba koma mwayi.
  • Ukapulumuka pa tsoka (zovuta) si bwino kuumirira mchitidwe womwe unakuchititsa kuti upezeke mu tsokalo popeza pambuyo pake ukhoza kutaya moyo kapena sungapulumukenso.
  • Papsa tonola, sudziwa mtima wa moto.
  • Ukapeza mwayi wochitira zina zake ndi bwino kugwiritsira ntchito mwayiwo.
  • (a) Mamveramvera adachotsa zolo pa ukwati.
    (b)Wawona nkhanga mawanga wataya nkhwali.
  • Ukamamvera zonena anthu mosaganizira bwino, umataya nazo mwayi womwe unali nawo kale.
  • Mako ndi mako usamuwone kuchepa mwendo.
  • Tizipereka ulemu kwa makolo ngakhale akhale onyozeka.
  • Konza kapansi kuti kam'mwamba katsike.
  • Munthu ukafuna kuti ena akuchitire zabwino yamba ndiwe kuwachitira zabwino.
  • Choka m'mbuyo khwangwala atole mphutsi.
  • Osachita zinthu motsekereza mwayi wa anthu ena.
  • Pita uko si kuyenda. Si bwino pamene muli paulendo umodzi kupangana kuti dzera uko chifukwa paulendo wotero kumavuta kukumana kwake.
    Mbalame zomamwera chigobi chimodzi zimadziwana nthenga. Anthu ochita zofanana amayendera limodzi ndi kudziwana kwambiri zochita zawo.
    (a) Uchembere n'kudyerana.
    (b) Kachipande katherere kakoma n'kuyenderana.
    (c) Lende (katungwe) n'kukankhana.
    (d) Mnzako akakuti konzu, nawe umam'ti konzu
    (e) Dombolo n'kuwombolana, nthengu adawombola njiwa.
    Tanthauzo: Zinthu zimakhala bwino kumathandizana osati m’modzi yekhayekhayo kumathandiza mnzake.
    Mapanga awiri avumbwitsa. Kuchita zinthu ziwiri nthawi imodzi kumapezetsa mavuto kapena kumalepheretsa zinthu kuti zichitike bwino.
    Taleka n'talawa adatha mphika. Munthu akaganiza zoyerekeza kuyamba kuchita chinthu, kumakhala kovuta kudziletsa kuchichita chinthucho chifukwa amafika pochizolowera.
    Mnzako akapsa ndevu mzimire mawa adzazima zako. Mnzathu akakhala pa mavuto tim'thandize popeza mawa lake akhoza kudzatithandiza ife.
    Akuluakulu ndi m'dambo mozimira moto. Akuluakulu ndiwo amathandiza zinthu zikafika povuta.
    Za kumzinda sawulula. Ndi bwino kuti tizisunga chinsinsi cha zimene tawona