Zining'a
Menu
Hide Menu

ZINING'A

Kodi chining'a ndi chiyani?

Chining'a ndi mawu amodzi kapena gulu la mawu ochepa onena mozimbayitsa ndipo ali ndi matanthauzo obisika. Anthu akafuna kukambirana nkhani zobisa, kapena zoti anthu ena asadziwe zomwe zikunenedwa; anthuwo amayankhula mophiphiritsa. Zining'a zimakometsa nkhani kotero zimachititsa awerengi kapena omvera kuti amve kukoma kwa chiyankhulo.

Zitsanzo za zining'a ndi matanthauzo ake

Chining'a

Tanthauzo

Bisa nkhope chita mlubza
Byala ufa mwalira
Chitsinzi munthu wochita zoyipa mobisa
Dothi lokhalokha anthu ambiri
Dziko kapena mudzi manda
Dzinthu kapena vinthu chakudya chambiri
Dzuwa .njala
Galu wakuda njala
Kalowam'malaya njala
Kabwere mawa chinthu chosalimba
Japani nsalu yotha msanga
Kubisala pachipandekunana
Kadam'manja munthu wosawuka
Mphemvu m'dyera ku mthiko munthu wosawuka
Kwakwatuke munthu wosawuka
Kamwendo m'njiramunthu woyendayenda
Matako akana pansimunthu woyendayenda
Wodya matako a galu munthu woyendayenda
Kaponda chimziri munthu woyendayenda
Kanga ndiwamba. munthu womana
Mphungu sataya nthengamunthu womana kwambiri
Kazitape munthu wodanitsa
M'thirakuwiri munthu wodanitsa
Kavuwevuwemunthu wodanitsa
Bwezera phala kum'kobwe kuchita zolepheretsa nzathu kuti asatichitirenso zabwino
Tsinira mafulufute kuuna kutsekereza zabwino
Dula phazi leka kupita pakhomo la munthu wina
Fundika bulangeti pusitsa
Gwira m'maso pusitsa
Phimba m'maso pusitsa
Yala udzu pusitsa
Kumuwaza mchenga m'maso kupusitsana
Gona pa lumbe gona osafunda kanthu
Igwa nkhopechita manyazi
Thyola bano kutha msinkhu/kukula/kuchoka pa ubuthu kukhala namwali
Gwilitsa fuwa lamoto kupusitsa munthu/kulindiritsa
Kumata phula m’masokunamiza mzako
Iwala gaga. mwalira
Kwatiwa n’kumbuyo komwe kukwatiwa ndi munthu wolemera
Kukwatiwa pantchafu kukwatiwa ndi munthu wosawuka.
Lerera mwana pachinena/pachilolo kulera momusasatitsa/momupusitsa
Kuloza ndege ndi chala nyada
Chotsa chimbenenechenjeretsa/khaulitsa
Nong’oneza bondo kudandaula utapeza mavuto chifukwa chosamvera
Tchera kumwezikuzindikira mofulumira za chinyengo cha munthu pamene munthuyo asadachite zomwe anakonzekera zokhudza chinyengocho
Thawa mtswatswa wako womwe dabwa/kukana zomwe unaziyamba iwe mwini
Tola nkhwangwa ndi mpini womwe chita mwayi waukulu